International News
Dziko la Sudan lipanga Ubale Ndi Zigawenga zama Gulu Asanu
![](https://www.mrbvibes.com/wp-content/uploads/2020/08/IMG-20200831-WA0025.jpg)
Dziko la Sudan lero lasainirana pangano la mtendere ndi gulu lazigawenga lochokera ku Darful.
Mwambowo udachitikira mdziko la South Sudan ndipo mkhara pakati adari Mtsogoleri wadziko la South Sudan Salva Kiir. Komanso Prime Minister wa Sudan Abdallah Hamdok ndi akuluakulu ena.
Mdziko la Sudan mwakhara mulinkhondo yapachiweniweni kwazaka khumi.
Anthu ambiri adafa komanso kuthawa mdzikolo zaka zambuyomu.